"ANYAMATA AKUPHONYA KWAMBIRI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake ikuchulutsa mipata yomwe akuphonya kwambiri zomwe zikupangitsa kuti azitaya mapointsi ambiri mmasewero awo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anafanana mphamvu ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Mpira ndipo wati anyamata ake sakudekha akafika pagolo.
"Anali masewero ovuta kwambiri, anzathuwa anasewera mchigawo choyamba pomwe ife mchigawo chachiwiri koma kungoti mipata yathu taphonya kwambiri, anyamatawa sakumadekha akafika pagolo." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe yapeza mapointsi okwana 32 pa masewero 24 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores