"TIKANAWINA KOMA OYIMBIRAWA SANAMAFUNA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Alick Chirwa, anachoka atakwiya pa bwalo la Mpira loweruka pomwe wati oyimbira amapanga ziganizo zofuna kuyipweteka timu yake pomwe imasewera ndi Bangwe All Stars.
Chirwa amayankhula izi atatha masewero omwe anafanana mphamvu 1-1 ndi zigoli za Levison Maganizo komanso James Tambwali ndipo wati kukonza kwawo kunali kuti apambane basi.
"Anali masewero ophweka kwambiri koma oyimbira amafuna kuti tizilimbana. Nokha mukuona chinthu akakukanirani molalo imatha nde timangokhala kumbuyo kuja poopa kuti awapatsa chigoli mwina cha offside." Anatero Chirwa.
Iye wati sanakhutire ndi zotsatirazi pomwe wati anakonza kuti apambane. KB ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 36 pa masewero 24.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores