MBAVA ZAKUMPIRA ZIONA MAVUTO
Zachinyengo ku masewero a mdziko muno zikuyembekezeka kutha pomwe bungwe la Football Association of Malawi yapanga mgwirizano ndi bungwe lothana ndi Katangale la Anti Corruption Bureau (ACB) mammawa a lolemba.
Mtsogoleri wa FAM, Walter Nyamilandu Manda, wati ndi mgwirizanowu zoipa zomwe zimachitika kumpira tsopano zichepa pomwe zambiri sizimabwera poyera.
Mkulu wa ACB, Martha Chizuma, wachenjeza kuti samvera chisoni wina aliyense koma olakwitsayo anjatidwa kuti alandire chilango. Iye wati amakanika kulowerera ku mpira kamba koti amasowa mpata ngati umenewu.
Komiti ya anthu khumi ipangidwa pansi pa mgwirizanowu ndipo zina mwa zomwe azifufuza ndi mmene osewera amatengedwera ku Flames, osewera kusintha matimu, za oyimbira komanso ndalama zapachipata.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores