"RED LIONS SI TIMU YOTI YATULUKA KAPENA YOPHWEKA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati wawauza osewera ake kuti asayiphweketse Red Lions ponena kuti akhale masewero ovuta kukumana nayo.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo omwe ali pa bwalo la Karonga lachitatu ndipo wati timu yawo ikufunikira mapointsi onse atatu kuti imalize pabwino mu ligiyi.
"Red Lions si timu yoti yatuluka kapena kuti mwina ikuvutika nde zikakhala zophweka ayi. Tawauza osewera kufunikira kopeza chipambano mmasewerowa ndipo lachitatu tikuyembekeza kuchita bwino." Anatero Kajawa.
Iye wati Nanson Mbewe yekha ndi yemwe sapezeka kamba koti ali ndi makadi achikasu atatu. Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi 33 pa masewero 23 mu ligi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores