"NZOVUTA KUFOTOKOZA, TAGONJA MOPWETEKA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake yagonja mmasewero awo omwe amatsogola 2-0 ndi Red Lions kamba koti anyamata ake anatayilira Poona kuti apambana kale.
Kajawa amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-2 pomwe anagoletsetsa zigoli zitatu mu mphindi zisanu zakumapeto ndipo wati ndi zinthu zovuta kuzimvetsetsa.
"Ndi Zovuta kufotokoza, tagonja tikutsogola 2-0 mpaka anzathu anabweramo, mwina anyamata anatayilira poyesa kuti apambana masewerowa koma zimangofunika kuti tingomalizitsa mpirawu sindikudziwa kuti chachitika ndi chani koma ndi mmene mpira umakhalira." Anatero Kajawa.
Kutsatira kugonjaku, Karonga ikhalabe pa nambala yachisanu ndi chimodzi pomwe ili ndi mapointsi 33 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores