"TAKONZA MAVUTO ATHU OMWE TINAPANGA NDI BULLETS" - KAMWENDO
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati timu yawo yaunikira bwino mavuto omwe anali nawo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets mkati mwa sabatayi ndipo abwera mosinthika pokumana ndi Kamuzu Barracks loweruka.
Kamwendo amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwa pa bwalo la Mpira ndipo wati ngakhale nthawi yokonzekera inali yochepa, iwo akwanitsa kuwauza anyamata zoyenerera.
"Tinasewera bwino ndi Bullets mwina tinachita kuwapatsa chigoli koma zonse zinali bwino vuto linali kuphonya kwambiri nde takonza zonsezo. Nthawi inali yochepa koma ntchito yake sinali yovuta ngati amakwanitsa kuyandikira golo, ziganizo ndi zomwe zimavuta, pomenya pagolo amapatsira, popatsira amamenya nde takonza." Anatero Kamwendo.
Bangwe ili pa nambala 8 pomwe ili ndi mapointsi 31 pa masewero 23 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores