"TIMU IKAGONJA SIKUTI IZINGOGONJABE" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wadzudzula mchitidwe wa anthu omwe akumayankhula kwambiri timuyi ikapanda kuchita bwino pomwe wati mu mpira matimu amaluzanso.
Iye amayankhula izi atagonjetsa timu ya Blue Eagles 2-1 pa bwalo la Dedza ndipo wati masewero awo anali ovuta koma chipambano chinali chofunika potseka pakamwa anthu oyankhula kwambiri.
"Vuto lake anthu amayankhula kwambiri, ineyo ndamenyapo mpira, nthawi zonse sikuti mukaluza ndekuti ndinu oluza basi nde komabe anyamata anaikapo mtima lero kuchokera kumbuyo mpaka tapambana." Anatero Chirwa.
Chipambano cha timuyi chaitengera pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ali ndi mapointsi 34 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores