"TAYENDA KWAMBIRI NDE TINALI TISANAMASUKE" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake inavutika kwambiri mchigawo choyamba ndi timu ya Bangwe All Stars kamba koti ulendo wawo waku DRC unali utawamanya osewera matupi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 ndipo anati kukonzekera kwawo sikunali kwa nthawi zonse koma wathokoza osewera atimuyi kamba kolimbikira ndi kupeza chipambano.
"Choyamba tithokoze osewera athu kamba ka chipambanochi, anali masewero ovuta kwambiri poti tikuchokera ku DRC nde tafika lamulungu anyamata sanapange zokonzekera bwinobwino nde matupi anali omangika koma mchigawo chachiwiri tasewera bwino mpaka tinapeza chigoli." Anatero Munthali.
Timuyi tsopano yabwera pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 43 pa masewero 20 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
870667416
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores