"TIGWIRITSA NTCHITO MASEWERO APAKHOMO BASI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake tsopano iyang'ana pa masewero anayi omwe yatsala nawo apakhomo kuti itsale mu ligi pomwe yatsakamira ku chigwa cha matimu otuluka mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Moyale Barracks ku Rumphi ndipo wati masewero apakhomo atsala nawo ambiri kusiyana ndi koyenda nde angolimbikira pakhomopo.
"Sikuti zinali zoyipa tikumapeza mipata koma tikuphonya kwambiri. Tatsala ndi masewero awiri koyenda ndipo ena onse ali pa khomo, tingogwiritsa ntchito mwayi osewerera pakhomopo kuti mwina titsale mu ligi." Anatero Chidati.
Civo yatsakamira pa nambala 14 mu ligi pomwe yatolera mapointsi okwana 25 pa masewero 24 omwe iyo yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores