"NGATI BANGWE TIKUNGOFUNA CHIPAMBANO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati sizikuwakhudza kuti timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili ndi mkwiyo ogonja mu CAF Champions league koma iwo akufuna mapointsi atatu basi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero omwe matimuwa akukumana pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo wati akudziwa kuti Bullets ndi yaikulu komanso osewera apangongole sasewera koma ali ndi anyamata ena aluso.
"Tikudziwa kuti Bullets ndi timu yaikulu komanso ndi mmene zachitikira kunja kuja afuna azitolere msanga koma ndife okonzeka. Ali ndi mphunzitsi wabwino komanso osewera apamwamba koma ifenso tili ndi osewera aluso, sitikuopa chifukwa tonse tili mu ligi." Anatero Mkandawire.
Atakumana mu gawo loyamba, Bullets inapambana 2-0. Bangwe All Stars ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri pomwe yatolera mapointsi 31 pa masewero 22.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores