"CHIBWANA NDI CHIMENE CHIKUMATIPWETEKA" - NYONI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati timu yake yagonja masewero ake ndi MAFCO mu ligi kamba ka chibwana pomwe wati akuphonya mipata kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndipo wati chibwana cha osewera akafika ku golo la anzawo, akumalangika nacho ku golo kwawo.
"Anali masewero abwino tinapeza mipata yoti tikanatha kupeza zigoli koma tinaphonya nde mukakumana ndi timu yoti ikufuna zigoli imakulanga kumapeto, mwina tizibwana pang'ono koma anyamata asewera bwino." Anatero Nyoni.
Sizikuyendabe ku Ekwendeni pomwe yafika pa nambala 12 ndi mapointsi 29 pa masewero 25 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores