"CHIGOLI TANGOWAPATSA KUTI ENI CHINYANI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati masewero omwe timu yake yagonja 1-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu ndi opweteka kwambiri kamba koti chigoli chake angopereka.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri koma aphonya mipata kamba kosowekera kudekha akafika malo oti atha kugoletsa.
"Zopweteka kwambiri, Bullets ndi timu yaikulu koma tinakwanitsa kuyisunga bwinobwino kungoti chigoli tangowapanga kuti eni chinyani. Tinapezadi mipata yabwino koma anyamata athu Sanathe kumenya bwino kuti agoletse." Anatero Mkandawire.
Timu ya Bangwe tsopano ili ndi 31 pointsi mu ligi ya TNM pomwe ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores