"KUMBUYO KWA WANDERERS SAMAYENDA NDE TINAPEZA MPATA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati kufanana mphamvu koyenda ndi timu ya Wanderers ndi zonyaditsa ndipo ziwathandizira pa nkhondo yawo yotsala mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anapeza chigoli mu mphindi zakumapeto kuti afanane mphamvu 1-1 ndipo wati anayiona Wanderers chofooka chomwe osewera ake anagwiritsa ntchito.
"Ndinayiona kuti Wanderers sikuyenda kumbuyo kwawo nde ndinawauza osewera kuti ayipanikizebe mchigawo chawo chomwecho mpaka zinatheka kuti tapeza chigoli chomwe ndi chofunikira kwambiri." Anatero Chingoka.
Moyale tsopano izipita mmasewero awo ndi Mighty Wakawaka Tigers lachitatuli ili pa nambala 11 ndi mapointsi 30 pa masewero 24.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores