"TIKUDABWA KUTI MPIRA WATHU UKUYENDA BWANJI" - KALINDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Ted Kalinda, wati wadabwa ndi uthenga woti timu yake yatuluka mu Airtel Top 8 chonsecho pa nkumano womwe unalipo masewero asanayambe anati akalepherana ifika ku mapenate.
Kalinda amayankhula izi atatha masewero omwe atuluka mu chikhochi angakhale kuti alepherana 1-1 ndi MAFCO ndipo wati chiganizo choti yochinya koyenda ipitilira chabwera kutangotsala mphindi zisanu.
"Ndikudabwa kuti akuti tatuluka malamulo azikhala mmene alili, ku mkumano masewero asanayambe anatikumbutsa kuti masewero kaya atha 1-1 kaya 0-0 afika ku mapenate koma kutatsala mphindi 5 ndi pomwe akuti zikatha chonchi MAFCO ipitilira." Anatero Kalinda.
Iye wati ngati kuli kukamang'ala pa nkhaniyi si mbali ya aphunzitsi a timuyi komatu akuluakulu a timuyi. Zateremu timuyi yatuluka mu chikhochi ndipo maso awo ayang'ana pa Castel Challenge Cup ndi TNM Supa ligi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores