"CIVO IKADALIPO MU LIGI" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, walimbitsa mtima otsatira timuyi kuti satuluka mu ligi ndipo awonananso chaka cha mawa.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi timu ya Red Lions 0-0 ndipo wati timu yake ikusewera bwino koma mwina pa nambala yomwe ali ikumawapatsa phuma mpake akumaphonya.
"Kumbali ya lero timu yasewera bwino koma mwina nambala imene tiki ikumatipatsa phuma. Ndiwauze ochemerera kuti masewero tikanali nawo, atatu pakhomo awiri koyenda nde tikanali mu ligi." Anatero Chidati.
Timu ya Civo ili ndi mapointsi 25 pa masewero 25 omwe yaseweranso mu ligi ndipo ili pa nambala 14 mu ligiyi.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores