"PENANSO OYIMBIRAWA AMATHANDIZA ANZATHUWA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati wavomereza kugonja poti timu yake inapereketsa zigoli zophweka kwambiri koma wati oyimbira anaithandizakonso Bangwe All Stars.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 pa bwalo la Mpira ndipo wati ziganizo zina zimasemphana ndi mmene zimafunikira komabe mavuto awo akonza.
"Inde chabwino tagonja koma pena tizinena chilungamo oyimbirawa ah pena ziganizo zawo zinali zokomera anzathuwa, ma offside awo samayimba komanso ma free kick omwe amawapeza anali abodza koma tavomereza, ndi Wanderers sitizabwereza zolakwa zathu." Anatero Chirwa.
Timuyi tsopano yatsika kufika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi 35 pa masewero 26 omwe yasewera mu ligiyi.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores