SCORCHERS YAFIKA NGATI MAFUMU
A Malawi ochuluka kwambiri anakhamukira mminsewu ya mzinda wa Blantyre kulandira timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi ya dziko lino kuchokera ku South Africa komwe apambana chikho cha COSAFA Women's Championship lero.
Timuyi yafika masana a lolemba kudzera pa bwalo la Chileka ndipo magalimoto ambiri, anthu odziwika ndi akuluakulu a boma anasonkhana pamodzi kufika pa bwaloli kuyilandira timuyi.
Iwo aonetsa chikhochi mu malo ngati Chileka, Kameza Roundabout, Chirimba, Che Mussa, Mbayani komanso ku msika waukulu wa Blantyre mpaka kukafika ku malo ogona a Sunbird Mount Soche ku Blantyre.
Iwo akhala ndi mwambo wa madyerero usiku wa lero pa malo ogonawa ngati njira yowalandira. Malawi inagonjetsa Zambia 2-1 kuti itenge chikhochi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores