FAM IKAMBIRANA ZA MPHUNZITSI WA FLAMES LERO
Komiti yaikulu ya bungwe la Football Association of Malawi ikumana mtsiku la lero ku Mpira house ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre kuti akambirane yemwe atenge ntchito ya mphunzitsi watimu ya Flames.
Izi zikudza pomwe timuyi ilibe mphunzitsi kamba koti mgwirizano wa Patrick Mabedi unatha mu September pomwe anatenga mmanja mwa Mario Marinica mu mwezi wa April.
Ndipo bungweli likuunikira dzina la Mabedi pamodzi ndi aphunzitsi 50 amdziko muno ndi akunja omwe analemberanso pa ntchitoyi kuti alowe mmalo mwa Marinica.
Timuyi ikhale ndi masewero mwezi wa mawa amu gulu lopitira ku mpikisano wa 2026 FIFA World Cup pomwe adzakumane ndi Liberia koyenda komanso Tunisia pakhomo.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores