"TABWERA KU BLANTYRE KUDZATENGA 3 POINTSI BASI" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake ya Silver Strikers yapita ku Blantyre ndi cholinga chimodzi chokha chomwe ndi kudzatenga mapointsi atatu pa mwamba pa timu ya Mighty Wakawaka Tigers.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu likudzali ndipo wati akudziwa kufunikira kopambana masewerowa kamba koti ligi tsopano ikufunikira kumatolera mapointsi.
"Zokonzekera zathu zayenda bwino, osewera ambiri omwe anali ovulala abwino, tikudziwa Tigers si, timalemekeze matimu omwe tikumenya nayo koma pomwe yafikira ligi yavuta kwambiri komabe tikupita ku Blantyre kuti tikatenge 3 pointsi." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver ili pa nambala yachitatu mu ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 43 pa masewero 24 omwe yasewera mu ligiyi ndipo akusiyana mapointsi anayi ndi FCB Nyasa Big Bullets yomwe ili pamwamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores