MAFUTA BWITIBWITI KU NTOPWA
Timu ya mpira wamiyendo koma ya atsikana ya Ntopwa Super Queens, yaponda mwala pomwe yapeza thandizo kuchokera ku kampani yopanga mafuta ya Capital Oil Refining pansi pa Kukoma Cooking Oil brand.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lachisanu pomwe yati tsopano dzina la timuyi lisintha ndipo izitchedwa Kukoma Ntopwa Super Queens kamba ka thandizoli.
Ndondomeko za mgwirizano wawo ziululika sabata ya mawa pomwe kukhale mwambo waukulu osainirana ma pepala pa mgwirizanowu.
Timuyi inachita mbiri yokhala timu yoyamba yaku Malawi kutenga nawo mbali mu chikho cha COSAFA CAF Women's Champions League womwe unachitikira ku South Africa ndipo mu timu ya Scorchers anatumizamo osewera atatu.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores