CHAWINGA WAGOLETSANSO KU PSG
Katswiri wa timu ya Scorchers, Tabitha Chawinga, akupitiliza kuchita bwino ku timu yake ya PSG pomwe loweruka wagoletsanso chigoli chake chachitatu ndi timuyi pomwe yagonjetsa Lille 4-0.
Chawinga anamwetsa chigoli chachiwiri cha timuyi mmasewerowa pomwe Katoto anali ataitsogoza kale ndipo Baltimore anamwetsa chigoli chachitatu kuti ikhale 3-0 popumulira.
Mchigawo chachiwiri, Vangsgaard anakhoma nsomali omaliza kuti timuyi ipambane mmasewerowa 4-0. Chawinga tsopano ali ndi zigoli zitatu zamuligiyi mmasewero anayi ndipo chimodzi ndi chamu UEFA champions league.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores