"PALIBE MWINI WAKE WA CHINTHU MU LIGIYI" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati iwo apitilizabe kumenya nkhondo kuti mwina china chake chichitika pomwe wati palibe mwini wake wa chinthu mu ligiyi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 2-2 ndi Blue Eagles ndipo wati ndi zopweteka poti achinyitsa kumapeto. Iye wati chimene ankafuna mu ligi anachipeza kwinaku ndi kungomenyera nkhondo basi.
"Ife chimene tinkafuna chinatheka komabe sizikutanthauza kuti tikhala chete, tipitilizabe kumenyera nkhondo poti palibe mwini wake wa chinthu mu ligiyi nde tiwalimbikitsabe osewerawa." Anafotokoza Mtetemera.
Timu ya Chitipa sinagonjebe pa bwaloli ngati akusewera pakhomo mu ligi ndipo yatsika kufika pa nambala yachinayi ndi mapointsi 43 pa masewero 24 mu ligiyi.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores