"SITIKUYANG'ANA ZA CHIKHO KOMA MASEWERO ALIWONSE" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wakana kuyikirapo mlomo pa nkhani yotenga chikho pomwe wati iwo amayang'ana za masewero omwe akusewera mtsiku limenelo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Mukuru Wanderers 1-0 pa bwalo la Bingu ndipo wati izi zilimbikitsa osewera kuti achite bwino mmasewero awo amtsogolo.
"Timanena kuti ngati osewera akudya bwino ndekuti azipambana masewero nde izi sizowakumbutsa mmasewero akubwerawa tilimbikira, ukachinya timu yaikulu umatayilira ukakumana ndi timu yaying'ono komabe zili ndi anyamatawa kuti achita bwanji." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver yafika pa nambala yachitatu pomwe yatolera mapointsi 43 pa masewero okwana 24 omwe asewera mu ligiyi.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores