"SITIKUYANKHULIRATU ZA CHIKHO KOMA TIPANGE ZA MASEWERO" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake tsopano sikuyang'ana zoti ikasewera masewero angapo iyandikira chikho koma iwo akupanga za masewero aliwonse pa okha.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Chitipa United 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake inali bwino pokwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri.
"Sitinganene kuti tavutika, tagoletsa zigoli ziwiri koma kungoti anzathuwa anabweranso ndi mtima woti akugonjetse paja anatichinya 1 koma leroli anyamata analimbikira tapambana 2. Sitikuyang'ana zoti tatsala ndi masewero motani, zambiri tidzayankhula mmasewero otsiriza amu ligi." Anatero Munthali.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikutsogolera ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 50 pa masewero 23 omwe yasewera ndipo yatsala ndi masewero awiri kuti afanane ndi omwe yamenya Wanderers yomwe ili pachiwiri.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores