"BULLETS INALI BWINO PA CHILICHONSE" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati kuchinyitsa changu mmasewero omwe amasewera ndi FCB Nyasa Big Bullets ndi kumene kwawapweteketsa pomwe wati ndi zovuta kuti kuchokera kumbuyo ndi matimu ngati amenewa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati Bullets inali bwino pa chilichonse angakhale kuti anyamata ake anayesetsa.
"Anzathuwa anachenjera chifukwa anagoletsa mwachangu nde ndi zovuta kwa timu ya masapota ochuluka chonchi kuti ungabwenze poti uyu ndi osewera wachi 12 nde awa ndi ana akadaphunzira anayesetsabe komabe Bullets inali bwino pa chilichonse." Anatero Mtetemera.
Masewero otsatira ndi okumana ndi timu ya Civo United lachitatu ndipo timuyi ikadali pachinayi ndi mapointsi okwana 43 pa masewero 25 omwe yasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores