PSG YA TABITHA YATOLA JOCKER
Timu ya PSG ya amayi yomwe kuli wosewera wa Scorchers, Tabitha Chawinga, ikuyembekezeka kukhala ndi ntchito yovuta kwambiri pomwe yaikidwa mu gulu lovuta kwambiri mu UEFA Women's Champions League lero.
Timuyi yaikidwa mu gulu C la mpikisanowu pamodzi ndi matimu a Bayern Munich yaku Germany, Roma yomwe ndi akatswiri aku Italy komanso timu ya Ajax yaku Netherlands.
Mayerewa anachitira mammawa a lachisanu ndipo timu ya PSG inazigulira malo ake mu ndime yamaguluyi itakwapula Manchester United 4-2 ndipo Chawinga anagoletsa ndi kuthandiza chigoli chimodzi mwa zinayizi.
Chawinga wakhala wosewera oyamba wa mpira wamiyendo wa amayi ku Malawi kusewera mu UEFA champions League, kugoletsa chigoli mu mpikisanowu komanso kusewera mu ndime yamagulu a chikhochi.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores