MAFCO YAFIKA MU NDIME YAMATIMU ANAYI MU AIRTEL TOP 8
Timu ya MAFCO yakhala yoyamba kuzigulira malo amu ndime ya matimu anayi amu chikho cha Airtel Top 8 kutsatira kulepherana 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks koma iwo apitilira kamba kogoletsa koyenda.
Dan Chimbalanga anamwetsa pa mphindi yoyamba yeniyeni koma Olson Kanjira anabwenza pa mphindi zinayi kuti masewero athere 1-1 zomwe zinasangalatsa mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti KB nayo inasewera bwino kwambiri koma tiyamike anyamata poti anachita zimene tinawauza zilibwino kuti tafika mu ndimeyi yomwe ndi yovuta kuti tikadutse koma chanzeru ndi choti tapitilira." Anatero Mwansa.
Timuyi tsopano idikilira matimu ena atatu omwe awatsatire mu ndimeyi ndipo imodzi idziwika lamulungu pomwe Blue Eagles ikulandira Moyale Barracks pa Nankhaka ndipo masewero ali 1-1.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores