Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"NZOTHEKA RED LIONS OSATULUKA MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula watsimikiza kuti ndi zotheka kuti timu yake isatuluke mu ligi koma zitengera mmene anyamata ake aziperekere mmasewero omwe atsala nawo.
Masapula amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Balaka ndipo wauza Sports Torch kuti timuyi ikungofunikira zipambano zingapo kuti ichoke kumunsi komwe iwo ali.
"Tikamasewera masewero timakhala ndi cholinga chimodzi, kuti tipambane masewerowa koma apa zikuvuta tagonja, tiyesetsa mmasewero atsalawa ndi ochepa koma titapambanako 4 kapena 5 mwina titha kuchoka kumunsi, sitingapeze osewera ena kuti asewere panopa, ndi omwewa nde tingowalimbikitsa kuti aike mtima." Anatero Masapula.
Red Lions yatsala ndi masewero okwana asanu ndi atatu (8) ndipo yatsakamirabe pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe yatolera mapointsi 18.
#Tawonga2023
CHESTER ANAGOLETSA CHIGOLI DZULO
Katswiri wa timu ya Flames, Yamikani Chester, anagoletsa chigoli chachiwiri cha timu yake ya Costa do Sol kuti ilepherane 2-2 ndi Ferroviario de Maputo loweruka lapitali.
Chigolichi chinabwera mu chigawo chachiwiri cha masewerowa ndipo Owinna itha kutsimikiza kuti Richard Mbulu ndi Chikoti Chirwa anayambanso mmasewero amenewa.
"OFFICIATION CHALLENGES NEED TO BE ADDRESSED" - KAYIRA
Former Flames and FCB Nyasa Big Bullets midfielder, Chimango Kayira, has said poor officiations by referees' in Malawi need to be addressed before it destroys something big.
Kayira wrote this on his Facebook page after incidents that happened at the Bingu National Stadium after Mighty Mukuru Wanderers protested a controversial Silver Strikers' goal leading to breaking of seats at the facility. Kayira says referees have been below par of late.
"The officiation challenges we are facing in our football needs to be addressed. Our beloved men in yellow have lately shown glimpses of inconsistency." Wrote Kayira.
In Silver Strikers vs Mighty Mukuru Wanderers match, referee Godfrey Nkhakananga awarded Silver Strikers a goal but after he had blown his whistle for a handball outside the box. Football Association of Malawi has withheld the results of the match.
TEMWA CHAWINGA, THOM NDI MADISE AFIKA KU SCORCHERS
Osewera atatu omwe amasewera kunja kwa dziko lino, Temwa Chawinga, Sabina Thom ndi Chimwemwe Madise tsopano afika mdziko muno patsogolo pa masewero omwe Scorchers ikumane ndi Seychelles lolemba pa bwalo la Mpira pokonzekera mpikisano wa COSAFA.
Osewerawa afika mdziko muno lamulungu pomwe akuyamba nawo zokonzekerazi ndipo asewera masewero ndi Seychelles lolemba ndi lachinayi.
Mtsogoleri wa timuyi, Tabitha Chawinga, sapezeka mu mpikisano wa COSAFA kamba koti wapita kumene ku timu yake ya PSG ku France.
baba tunde
denza danamod_ft burs
"BULLETS ILI NDI 75% MWAYI OTENGA LIGI" - KAMAU
Mmodzi mwa anthu oyankhulapo pa nkhani zamasewero mdziko muno, Kim Kamau, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili ndi mwayi onse oti itenge ligi ya TNM ndipo ichita kuchitaya okha.
Kamau amayankhula izi kutsatira mmene matimu anayi akupikisana pa chikhochi akuchitira ndipo wati timu ya Bullets ili ndi 75 percent mwayi otenga ligiyi ndipo enawa akugawana 25 yotsalayo.
"Chitipa inali ndi masewero awiri basi inapambana amodzi, Wanderers nayo inafanana mphamvu aja apa yagonjetsa Karonga, Silver ndi zimene tikunenazo pomwe Bullets yatsalabe ndi masewero. 75% Bullets itenga chikhochi, 15% ya Wanderers ndipo 7.5% kwa Chitipa ndi Silver kukwanitsa 100%." Anatero Kamau.
Bullets ili pa mwamba pa ligi ya TNM ndi mapointsi 40 angakhale kuti ikutsalira ndi masewero awiri kuti ifanane ndi Wanderers, Chitipa ndi Silver Strikers.
That's true am with you kimu
"AWA AKHALA MAYESERO KUTI TIDZIWE POMWE TITHERE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati masewero atimuyi pakati pa Red Lions lero komanso ndi Mighty Mukuru Wanderers lachitatu likudzali ali ngati mayesero kwa iwo kuti awaone mbali imene athere mu ligi ya chaka chino.
Kananji amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Red Lions pa bwalo la Balaka ndipo wati akuyembekeza kuti masewero awo akhala ovuta kwambiri. Iye wati akapambana masewero awo awiriwa atsimikizadi kuti satuluka mu ligi.
"Akhala masewero ovuta kamba koti tonse tikuvutika komanso titakumana pa Nankhaka tinalepherana 1-1 komabe anyamata tawauza kufunikira kopeza chipambano mmasewero awa ndi a Wanderers chifukwa ali ngati mayesero kuti tione mbali yomwe tithere. Tikapambana onse, zotuluka mu ligi sizitikhudza nawo." Kananji anafotokoza.
Timu ya Blue Eagles ili pa nambala 10 mu ligi ya chaka chino pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 22 ndipo ngati ipambane lero, ifika pa nambala 10.
Ghezay
Nomad
Video
bulets topu 8 ikutega basi maule mofaya
ine dimasapota maule kuno ku mozambique
SALIMA SAPITA NAWO KU SAUDI ARABIA
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets yemwe ali pangongole ku Bangwe All Stars, Chikumbutso Salima, sapita nawo mdziko la Saudi Arabia kuti akayese mwayi ku timu ya Al-Faisaly pomwe Bullets yakaniza osewerayu.
Izi zadziwika ndi mkulu watimuyi, Mphatso Jika, yemwe wati Salima anaikidwa pa ndandanda wa osewera atatu omwe iwo anapemphedwa kuti apereke ndi kuti akayese mwayi koma Bullets yakaniza kamba koagwirizana ndi ndondomeko zina za ulendowu.
Osewera atatu tsopano, Robert Saizi, Emmanuel Lino komanso mtsogoleri watimuyi, Fanizo Mwansambo ndi omwe akupita pa ulendowu womwe anyamuke lolemba likudzali.
Timu ya Bangwe ikumana ndi timu ya Bullets lachitatu sabata ya mawa ndipo osewera onse omwe anachoka ku Bullets kuphatikiza Salima sadzasewera masewerowa.
OFFICIAL
Martin Odegaard has signed a new contract with Arsenal until 2028.
KADENGE AKALOWA MMALO MWA DE JONGH
Mphunzitsi wakale watimu ya Ekwendeni Hammers, Edson Kadenge Mwafulirwa, waitanidwanso kutimu ya Silver Strikers patapita miyezi iwiri chimuimitsireni kuti akalowe mmalo mwa mphunzitsi watimuyi, Peter De Jongh, yemwe walowera mdziko la Kenya
Mmodzi mwa akuluakulu a komiti yaikulu ya timuyi, Willard Chakanika, watsimikiza za kuchoka kwa De Jong kamba koti chitupa chake chogwirira ntchito mdziko la Malawi Chatha mphamvu. Iye wati kusowa kwa ndalama yakunja kwachititsa kuti Silver ichedwe kupangitsanso chitupachi pomwe amafuna ndalama zokwana $2,000 yomwe ikukwana K2.5 million.
Kadenge, yemwe anaimitsidwa ndi timuyi kamba ka nkhani yomwe De Jongh ankati analedzera tsiku la masewero, atsogolera Mabanka mmasewero omwe akumane ndi Mighty Mukuru Wanderers mu chikho cha Airtel Top 8.
Malawi has maintained their position number 123 in the latest World FIFA Rankings.
PAJA WAMKULU AKAVUTIKA AMAMUTHANDIZIRA"" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets yachita kuthandizidwa ndi oyimbira kuti apambane mmasewero omwe matimuwa anakumana pomwe wati penate yomwe Bullets inapeza ndi yopatsidwa.
Nyambose amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Kamuzu pomwe Bullets yapambana ndi chigoli cha pa mphindi 88 za masewerowa kudzera pa penate. Iye wati timu yake yaphonya kwambiri komabe oyimbira wayithandiza Bullets.
"Ndi Zoona mchigawo choyamba tinasewera bwino kwambiri ndipo timapanga chilichonse koma mipata yathu sitinaigwiritse ntchito zomwe zinawathandiza anzathuwa kuti abweremo ndipo chigawo chachiwiri anali bwino komabe paja wamkulu ndi wamkulu akavutika amathandizidwa nde amuthandizadi." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers tsopano ikadali pa nambala 11 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
"MMASEWERO ALIWONSE OSEWERA AKUMAVULALA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wadandaula kuti timu yake ikumaluzako osewera mmasewero aliwonse kamba kuvulala chifukwa choti akusewera masewero ambiri pafupifupi.
Munthali amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Mighty Wakawaka Tigers 1-0 kuti ifike pamwamba pa ligi ya TNM ndipo wati masewerowa anali ovuta komabe akupitilira kuluza osewera.
"Tigers inasewera bwino mchigawo choyamba anali paliponse koma mchigawo chachiwiri tinabwera tinayesetsa mpaka tinapeza chigoli. Masewero achulukadi ndipo masewero aliwonse tikuluza osewera, lero Eric [Kaonga] wavulalanso oti anali konkonso, Sambani nayenso ndi ovulala, Fodya ndi uja amumanga mmutu nde sizilibwino." Anatero Munthali.
Bullets tsopano yachotsa timu ya Mighty Mukuru Wanderers pamwamba pa ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 40 ngakhale kuti ikutsalira ndi masewero awiri pa matimu omwe akupikisana nawo.
SENAJI NDI PHIRI SAPEZEKA NDI TIGERS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets sikhala ndi akatswiri awo awiri, Clyde Senaji ndi Precious Phiri pa masewero omwe akukumana ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu pomwe anavulala mmasewero awo ndi TP Mazembe mu CAF Champions League.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu, Heston Munthali, watsimikiza za nkhaniyi patsogolo pa masewerowa ndipo wati akudziwa kuti masewero a Tigers sakhala ophweka. Iye wati kumenya mipikisano yambiri ndi yosokoneza osewera ndipo ena akumavulala.
"Padakali pano tikusintha kupita ku TNM Supa ligi ndi maseweredwe enanso nde osewera tikuwaphunzitsa zinthu zisiyanasiyana nthawi imodzi komabe tawauza kufunikira kopambana masewero amenewa. Masewero aliwonse tikuluza osewera, ndi TP Mazembe Senaji ndi Precious Phiri anavulala komabe osewera ena azikhala okonzeka kugwira ntchito." Anatero Munthali.
Atakumana mchigawo choyamba, matimuwa anafanana mphamvu 1-1. Timu ya Bullets ili ndi mapointsi 37 pa nambala yachiwiri pomwe Tiger
"TIKUYANG'ANABE ZOTENGA LIGI" - MPINGANJIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Albert Mpinganjira, wati timu yawo ilimbikirabe kuti ikhale pamwamba pa ligi ya TNM pomwe akuyang'ana ukatswiri wa ligiyi ndipo wati masewero osaseweredwa si mapointsi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 2-1 ndi Karonga kuti afike pamwamba pa ligiyi ndipo anayamikira osewera ake kamba kulimbikira kuti apambane ndipo wati nawo akuyang'ana chikhochi.
"Pakadali pano tili pamwamba pa ligi, inde anzathu atsala ndi masewero ambiri osaseweredwa komabe si mapointsi amene nde kwa timu iliyonse mu ligi imakhumbira kutenga chikho, ifenso tikuyang'ana chikhochi." Anatero Mpinganjira.
Christopher Kumwembe anamwetsa zigoli ziwiri mu chigawo chachiwiri kuti abwenze chigoli cha Gabinho Daudi zomwe zathandiza Manoma kufika pa mapointsi 40 pa masewero 21.
Scorchers captain, Tabitha Chawinga, has joined French giants, Paris Saint German, from Wuhan Jiangda University of Chinese Women's Football league.
The loan deal is for a period of one year.
NYONDO WAYAMBA ZOKONZEKERA PATSOGOLO PA BULLETS
Katswiri wa timu ya Dedza Dynamos, Clement Nyondo, akuyembekezeka kubwereranso pa bwalo lazamasewero kumapeto a sabata ino pomwe wayamba zokonzekera ndi timuyi patsogolo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets mu chikho cha FDH Bank.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi pomwe yati osewera onse atimuyi ali bwino tsopano ndipo akupanga zokonzekera ndi timuyi patsogolo pofuna kuzigulira malo mu ndime yotsiriza ya chikhochi.
Goloboyi wa timuyi, Donnex Mwakasinga, yemwe anathamangira naye ku chipatala sabata yatha atavulala mmasewero ndi Silver Strikers tsopano alibwino, Chifuniro Mpinganjira yemwenso anali ovulala wabwerera chimodzimodzi Okhaya Okot Otim ndi Clement Nyondo alinso bwino.
Aka kakhala kachiwiri matimuwa akukumana pomwe mu ligi ya TNM pa bwalo la Kamuzu, matimuwa analepherana 2-2 ndipo Nyondo ndi yemwe anagoletsakonso mmasewerowa.
"TINACHITAYA MU CHIGAWO CHACHIWIRI" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati kugonja kwa timu yake ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu ligi ya TNM ndi chifukwa choti mu chigawo chachiwiri sanasewere bwino.
Kajawa amayankhula izi atatha masewerowa omwe agonja 2-1 ndipo timuyi imatsogola mchigawo choyamba koma Christopher Kumwembe anamwetsa zigoli ziwiri mu chigawo chachiwiri kuti Manoma apambane. Iye wati mchigawo chachiwiri sanasewere bwino.
"Tagonja inde komabe anyamata asewera bwino, anayesetsa komabe mchigawo chachiwiri zinativuta pomwe mwina amakhutira kuti akutsogola pomwe anakhazikika kumbuyo ngakhale kuti sitinawauze zimenezo. Tivomereze kuti zativuta ndithu." Anatero Kajawa.
Kugonja kumeneko ndi koyamba kwa mphunzitsiyu kutimuyi yomwe ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 31 pa masewero 22 mu ligiyi.
"TIMU NGATI WANDERERS IMAFUNIKIRA CHIKHO CHAKA CHILICHONSE" - KUMWEMBE
Katswiri watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, wati sakuyang'ana kuti akupeza zigoli motani koma kuti timu izichita bwino pomwe wati timu yaikulu ngati Wanderers sifunika kutuluka opanda chikho.
Kumwembe anayankhula izi atasankhidwa kukhala osewera wapamwamba mmasewero omwe Wanderers yagonjetsa Karonga United 2-1 ndipo iye anamwetsa zigoli ziwiri. Iye anati kuvulala ndi kumene kunamusokoneza koma amadziwa kuti abwereramo.
"Sindimayang'ana kuti ndifike pati koma kukhala kumbali yoluza zimawawa nde mmene masapota amakuwira zinandilimbikitsa kuti ndipeze zigolizi. Kuvulala kunandisokoneza ndakhala mwezi osamenya mpira komabe ndizitolera bwinobwino." Anatero Kumwembe.
Katswiriyu wakhala pafupifupi miyezi itatu osagoletsa chigoli chilichonse mu ligi ya TNM koma tsopano ali ndi zigoli 9 ndipo akuchepekedwa ndi zigoli zinayi kuti amupeze Clement Nyondo.
Fcb bulents
"TIKUKUMANA NDI WANDERERS YOKWIYA KOMA SITIKUSAMALA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati masewero atimu yake ndi Mighty Mukuru Wanderers akhala ovuta kwambiri potengera kuti Wanderers ili yokwiya ndi zotsatira za masewero awo awiri apitawa.
Kajawa amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe achitikire pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo iye wati timu yake yakonzeka kukalimbana ndi Manoma mmasewero ovuta kwambiri.
"Ifeyo takonzeka, tikudziwa kuti Wanderers sibwera mophweka chifukwa choti sinachite bwino mmasewero awiri apitawa koma ndi mmene tachitira mmasewero anayi apitawa nafe timu yake ikuonetsa kuti siyophwekanso. Iwo abwera mokwiya koma sitikusamala, tilimbana nawo mpaka titenge 3 points." Anatero Kajawa.
Timu ya Karonga United sinagonjeko chibwerereni Kajawa kutimuyi ndipo ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 32 pa masewero 21 omwe yasewera mu ligiyi.
CASTEL IBONGA POMWE MAYERE ALIKO MAWA
Matimu 16 amu TNM Supa ligi tsopano adziwa matimu omwe akumane nawo mu chikho cha Castel Challenge Cup pomwe mayere a ndime ya matimu 64 achikhochi achitika mawa ku Mpira house ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi limene lapereka uthengawu pomwe tsopano matimu okwana 64 a mbali zisiyanasiyana akumane tsopano.
Matimu 16 amu TNM Supa ligi apahtikizana ndi matimu 17 amu zigawo zonse za dziko lino ndipo enanso 31 a mmizinda ya dziko lonse atenga nawo mbali mmayerewa.
Mayerewa adzayamba nthawi ya 10:00 ku mmawa. Ichi ndi chaka choyamba kuchitika mpikisanowu omwe wakhudza matimu odutsa 2,000.
SCORCHERS ISEWERA MASEWERO AUBALE NDI SEYCHELLES
Timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi, the Scorchers, yachita mwayi opeza masewero aubale ndi timu ya Seychelles patsogolo pa mpikisano wa COSAFA Women's Championship omwe uyambe mwezi wa mawa.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi limene latsimikiza za nkhaniyi ndipo wati masewerowa adzaseweredwa kawiri pomwe matimuwa adzakumane pa 25 September lomwe ndi lolemba komanso lachinayi pa 28 September.
Masewero onse awiri adzachitikira ku bwalo la Mpira ku Chiwembe ku Blantyre ndipo Seychelles ikuyembekezeka kufika mdziko muno loweruka pa 23 September 2023.
Timu ya Malawi inalowa mu m'bindikiro lamulungu pomwe ikonzekera mpikisanowu omwe uyambe pa 4 October mpaka 15 October 2023.
TABITHA CHAWINGA AKUPITA KU PSG
Katswiri wa Scorchers, Tabitha Chawinga, akubwereranso ku Ulaya pomwe wasaina mgwirizano wa chaka chimodzi wapangongole ndi timu yaku France ya PSG.
Katswiriyu wasaina mgwirizano wakeyu dzulo ndipo mkhalapakati wake wa mdziko muno, Theana Msolomba, watsimikiza za nkhaniyi.
"Panali matimu ambiri omwe amamufuna koma titaunikira tinaona kuti yopita ku PSG pangongole ndi imene ili bwino. Tinafunanso kuti zofuna za timu yake ya Wuhan Jiangda University zisapwetekedwe." Anatero Msolomba.
Tabitha analinso pangongole kutimu ya Inter Milan ku Italy kuchokera chaka chatha koma Wuhan inakana kuonjezera kapena kuti Inter imusainiretu.
Zambiri za mu mgwirizanowu sizinatulutsidwe ati kamba koti mbali zonse zokhudziwa zikadakambiranabe pa nkhaniyi.
SAIZI, SALIMA NDI LINO AKUPITA KU SAUDI ARABIA
Osewera atatu a Bangwe All Stars, Robert Saizi, Emmanuel Lino ndi Chikumbutso Salima, yemwe ali pa ngongole kuchokera ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets akulowera mdziko la Saudi Arabia komwe akukayesa mwayi kumeneko.
Mkulu wa timuyi, Mphatso Jika, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati timu ya Al-Faisaly yomwe imasewera mu ligi yaying'ono yachiwiri ku dzikoli ndi imene yawaitana osewerawa.
"Timadikira kuti atitumizire makalata owapempha osewerawa kuti apite ndipo afika lachisanu la sabata yatha. Ndili ndi chikhulupiliro kuti osewerawa akachita bwino ndipo akatsala mdzikomo." Anatero Jika.
Osewerawa akuyembekezeka kunyamuka mdziko muno pa 25 September lomwe ndi lolemba sabata yatha. Saizi ndi Salima akhala akuchita bwino kutimuyi ndi Flames yomwe pamene Lino ndi yemwe wakhala odalilika kutsogolo kwa timuyi.
Source: Times #Tawonga2023
MGHT WANDRALES VS MAFUKO
MGHT VS MAFUKO
"SILVER SINGATENGE LIGI CHIFUKWA CHA DE JONGH" - KAYIRA
Katswiri wakale wosewera mpira wamiyendo, Peterkins Kayira, wati mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter De Jongh, ndi chifukwa chachikulu chimene timuyi singatengere ukatswiri wa ligi kamba koti anapha mzimu wopambana kwa osewera.
Kayira wayankhula izi pa Times 360 ndipo wati De Jongh si wa mpira kamba koti amawabwenzeretsa mmbuyo osewera kuti alimbikire.
"Ineyo ndinayichotsa kalekale Silver potenga ligi vuto lake ndi kochi, mulibemo zampira ndipo ndi yemwe wapha mzimu opambana mwa osewera. Pa zaka zonsezi fufuzani kuti Silver yapeza makadi ambiri mu ligi yake iti? Ndi inoyi, mmene amawapangira osewera sangapambane." Anatero Kayira.
Koma mzake, Pally Chinyama, anatsutsana naye kunena kuti osewera atimuyi alibe mtima omenyera mpaka kumapeto ngati osewera a FCB Nyasa Big Bullets. Silver ili pa nambala yachinayi pomwe ili ndi mapointsi 36 pa masewero 22.
👍 Person in charge
"SIZINAYAMBE KUOPSA KWENIKWENI" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati sizinayambe kuopsa kwenikweni ku mbali yawo kuti atha kumadera nkhawa zoti atha kutuluka angakhale kuti zotsatira zikuvuta kutimuyi.
Nyoni amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zigoli zomwe anagoletsetsa zinali zachangu koma amaliza bwino zomwe zikuwapatsa mphamvu.
"Sizinayambe kuopsa kwenikweni, batani la chiopsezo sitinadine nde timenyabe kuti tiyambe kuchita bwino, tasewera bwino makamaka kumapeto nde ndi mmene tathera, titenga zimenezo kuzipititsa mmasewero athu otsatira, ndi achisodzera ndipo akadaphunzira." Anatero Mauluka.
Iye wati akonza molakwika kuti mmasewero awo otsatira adzachite bwino. Hammers ikadali pa nambala 9 pomwe ili ndi mapointsi 28 pa masewero 22 omwe asewera.
"SIKUTI ZAYERA KOMA TICHILIMIKABE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake sinapezebe mtendere ndipo akuyenera kuchilimika angakhale atalikirana ndi nambala za matimu otuluka mu ligi.
Kananji amayankhula izi atatha masewero omwe apambana 2-1 ndi timu ya Ekwendeni Hammers pa bwalo la Nankhaka ndipo wati anawapempha osewera ake kuti apambane chifukwa Ekwendeni imawavuta kwambiri.
Iye wati anyamata ake akumvera zimene akuuzidwa koma wati asatayilire chifukwa mtendere sunawachokere.
"Yakhala ili nyimbo kuti tikuyenera kuchoka kumunsi tili kuja nde padakali pano ligi yavuta nde anyamata sakuyenera kugona komabe tikuyesetsa kuti tichokeretu." Anatero Kananji.
Timu ya Blue Eagles yafika pa nambala 10 mu ligiyi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 27 pa masewero 22 amu ligiyi.
"MU MASEWERO A CIVO ANAWABERA, TENGANI CHITSANZO CHINA" - KAYIRA
Katswiri wakale wa timu ya Flames, Peterkins Kayira, wati chitsanzo choti timu ya FCB Nyasa Big Bullets imatha kuchokera kumbuyo ndi kupambana chisakhale ndi masewero omwe anapambana 3-2 ndi Civo kamba koti zigoli ziwiri za Bullets zinali zabodza.
Kayira amayankhula izi pa Times 360 ndipo wati zigoli za Bullets ziwiri za mmasewero awo ndi Civo zinali zabodza. Iye wati masewero omwe Bullets yagonja 1-0 ndi TP Mazembe inachita kufuna yekha.
"Kugonja kwa Bullets kunali kofuna chifukwa zolakwika zimene amapanga zinali zotheka osazipanga. Bullets inachulutsa ulemu kwambiri kuchokera pachiyambi ndipo Mazembe itapeza chigoli imatha kusewera bwino kuusintha mpira ndipo goloboyi si nthawi yogoletsetsa chigoli." Anatero Kayira.
Komabe iye wati mmene inasewera Bullets palibe timu ya mdziko muno ikanalimba ndipo ngati angakonze mavuto awo, ikhonza kukawina. Bullets ikumana ndi TP Mazembe mu masewero achiwiri pa 30 September ku DR
FDH Bank Cup