"SIZINAYAMBE KUOPSA KWENIKWENI" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati sizinayambe kuopsa kwenikweni ku mbali yawo kuti atha kumadera nkhawa zoti atha kutuluka angakhale kuti zotsatira zikuvuta kutimuyi.
Nyoni amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zigoli zomwe anagoletsetsa zinali zachangu koma amaliza bwino zomwe zikuwapatsa mphamvu.
"Sizinayambe kuopsa kwenikweni, batani la chiopsezo sitinadine nde timenyabe kuti tiyambe kuchita bwino, tasewera bwino makamaka kumapeto nde ndi mmene tathera, titenga zimenezo kuzipititsa mmasewero athu otsatira, ndi achisodzera ndipo akadaphunzira." Anatero Mauluka.
Iye wati akonza molakwika kuti mmasewero awo otsatira adzachite bwino. Hammers ikadali pa nambala 9 pomwe ili ndi mapointsi 28 pa masewero 22 omwe asewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores