SENAJI NDI PHIRI SAPEZEKA NDI TIGERS
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets sikhala ndi akatswiri awo awiri, Clyde Senaji ndi Precious Phiri pa masewero omwe akukumana ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu pomwe anavulala mmasewero awo ndi TP Mazembe mu CAF Champions League.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu, Heston Munthali, watsimikiza za nkhaniyi patsogolo pa masewerowa ndipo wati akudziwa kuti masewero a Tigers sakhala ophweka. Iye wati kumenya mipikisano yambiri ndi yosokoneza osewera ndipo ena akumavulala.
"Padakali pano tikusintha kupita ku TNM Supa ligi ndi maseweredwe enanso nde osewera tikuwaphunzitsa zinthu zisiyanasiyana nthawi imodzi komabe tawauza kufunikira kopambana masewero amenewa. Masewero aliwonse tikuluza osewera, ndi TP Mazembe Senaji ndi Precious Phiri anavulala komabe osewera ena azikhala okonzeka kugwira ntchito." Anatero Munthali.
Atakumana mchigawo choyamba, matimuwa anafanana mphamvu 1-1. Timu ya Bullets ili ndi mapointsi 37 pa nambala yachiwiri pomwe Tiger
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores