"MMASEWERO ALIWONSE OSEWERA AKUMAVULALA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wadandaula kuti timu yake ikumaluzako osewera mmasewero aliwonse kamba kuvulala chifukwa choti akusewera masewero ambiri pafupifupi.
Munthali amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Mighty Wakawaka Tigers 1-0 kuti ifike pamwamba pa ligi ya TNM ndipo wati masewerowa anali ovuta komabe akupitilira kuluza osewera.
"Tigers inasewera bwino mchigawo choyamba anali paliponse koma mchigawo chachiwiri tinabwera tinayesetsa mpaka tinapeza chigoli. Masewero achulukadi ndipo masewero aliwonse tikuluza osewera, lero Eric [Kaonga] wavulalanso oti anali konkonso, Sambani nayenso ndi ovulala, Fodya ndi uja amumanga mmutu nde sizilibwino." Anatero Munthali.
Bullets tsopano yachotsa timu ya Mighty Mukuru Wanderers pamwamba pa ligiyi pomwe ili ndi mapointsi 40 ngakhale kuti ikutsalira ndi masewero awiri pa matimu omwe akupikisana nawo.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores