SAIZI, SALIMA NDI LINO AKUPITA KU SAUDI ARABIA
Osewera atatu a Bangwe All Stars, Robert Saizi, Emmanuel Lino ndi Chikumbutso Salima, yemwe ali pa ngongole kuchokera ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets akulowera mdziko la Saudi Arabia komwe akukayesa mwayi kumeneko.
Mkulu wa timuyi, Mphatso Jika, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati timu ya Al-Faisaly yomwe imasewera mu ligi yaying'ono yachiwiri ku dzikoli ndi imene yawaitana osewerawa.
"Timadikira kuti atitumizire makalata owapempha osewerawa kuti apite ndipo afika lachisanu la sabata yatha. Ndili ndi chikhulupiliro kuti osewerawa akachita bwino ndipo akatsala mdzikomo." Anatero Jika.
Osewerawa akuyembekezeka kunyamuka mdziko muno pa 25 September lomwe ndi lolemba sabata yatha. Saizi ndi Salima akhala akuchita bwino kutimuyi ndi Flames yomwe pamene Lino ndi yemwe wakhala odalilika kutsogolo kwa timuyi.
Source: Times #Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores