"BULLETS ILI NDI 75% MWAYI OTENGA LIGI" - KAMAU
Mmodzi mwa anthu oyankhulapo pa nkhani zamasewero mdziko muno, Kim Kamau, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili ndi mwayi onse oti itenge ligi ya TNM ndipo ichita kuchitaya okha.
Kamau amayankhula izi kutsatira mmene matimu anayi akupikisana pa chikhochi akuchitira ndipo wati timu ya Bullets ili ndi 75 percent mwayi otenga ligiyi ndipo enawa akugawana 25 yotsalayo.
"Chitipa inali ndi masewero awiri basi inapambana amodzi, Wanderers nayo inafanana mphamvu aja apa yagonjetsa Karonga, Silver ndi zimene tikunenazo pomwe Bullets yatsalabe ndi masewero. 75% Bullets itenga chikhochi, 15% ya Wanderers ndipo 7.5% kwa Chitipa ndi Silver kukwanitsa 100%." Anatero Kamau.
Bullets ili pa mwamba pa ligi ya TNM ndi mapointsi 40 angakhale kuti ikutsalira ndi masewero awiri kuti ifanane ndi Wanderers, Chitipa ndi Silver Strikers.
#Tawonga2023
That's true am with you kimu
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores