"TIKUKUMANA NDI WANDERERS YOKWIYA KOMA SITIKUSAMALA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati masewero atimu yake ndi Mighty Mukuru Wanderers akhala ovuta kwambiri potengera kuti Wanderers ili yokwiya ndi zotsatira za masewero awo awiri apitawa.
Kajawa amayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe achitikire pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo iye wati timu yake yakonzeka kukalimbana ndi Manoma mmasewero ovuta kwambiri.
"Ifeyo takonzeka, tikudziwa kuti Wanderers sibwera mophweka chifukwa choti sinachite bwino mmasewero awiri apitawa koma ndi mmene tachitira mmasewero anayi apitawa nafe timu yake ikuonetsa kuti siyophwekanso. Iwo abwera mokwiya koma sitikusamala, tilimbana nawo mpaka titenge 3 points." Anatero Kajawa.
Timu ya Karonga United sinagonjeko chibwerereni Kajawa kutimuyi ndipo ili pa nambala yachisanu ndi mapointsi 32 pa masewero 21 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores