TABITHA CHAWINGA AKUPITA KU PSG
Katswiri wa Scorchers, Tabitha Chawinga, akubwereranso ku Ulaya pomwe wasaina mgwirizano wa chaka chimodzi wapangongole ndi timu yaku France ya PSG.
Katswiriyu wasaina mgwirizano wakeyu dzulo ndipo mkhalapakati wake wa mdziko muno, Theana Msolomba, watsimikiza za nkhaniyi.
"Panali matimu ambiri omwe amamufuna koma titaunikira tinaona kuti yopita ku PSG pangongole ndi imene ili bwino. Tinafunanso kuti zofuna za timu yake ya Wuhan Jiangda University zisapwetekedwe." Anatero Msolomba.
Tabitha analinso pangongole kutimu ya Inter Milan ku Italy kuchokera chaka chatha koma Wuhan inakana kuonjezera kapena kuti Inter imusainiretu.
Zambiri za mu mgwirizanowu sizinatulutsidwe ati kamba koti mbali zonse zokhudziwa zikadakambiranabe pa nkhaniyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores