TEMWA CHAWINGA, THOM NDI MADISE AFIKA KU SCORCHERS
Osewera atatu omwe amasewera kunja kwa dziko lino, Temwa Chawinga, Sabina Thom ndi Chimwemwe Madise tsopano afika mdziko muno patsogolo pa masewero omwe Scorchers ikumane ndi Seychelles lolemba pa bwalo la Mpira pokonzekera mpikisano wa COSAFA.
Osewerawa afika mdziko muno lamulungu pomwe akuyamba nawo zokonzekerazi ndipo asewera masewero ndi Seychelles lolemba ndi lachinayi.
Mtsogoleri wa timuyi, Tabitha Chawinga, sapezeka mu mpikisano wa COSAFA kamba koti wapita kumene ku timu yake ya PSG ku France.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores