SCORCHERS ISEWERA MASEWERO AUBALE NDI SEYCHELLES
Timu ya mpira wamiyendo koma ali amayi, the Scorchers, yachita mwayi opeza masewero aubale ndi timu ya Seychelles patsogolo pa mpikisano wa COSAFA Women's Championship omwe uyambe mwezi wa mawa.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi limene latsimikiza za nkhaniyi ndipo wati masewerowa adzaseweredwa kawiri pomwe matimuwa adzakumane pa 25 September lomwe ndi lolemba komanso lachinayi pa 28 September.
Masewero onse awiri adzachitikira ku bwalo la Mpira ku Chiwembe ku Blantyre ndipo Seychelles ikuyembekezeka kufika mdziko muno loweruka pa 23 September 2023.
Timu ya Malawi inalowa mu m'bindikiro lamulungu pomwe ikonzekera mpikisanowu omwe uyambe pa 4 October mpaka 15 October 2023.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores