"NZOTHEKA RED LIONS OSATULUKA MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula watsimikiza kuti ndi zotheka kuti timu yake isatuluke mu ligi koma zitengera mmene anyamata ake aziperekere mmasewero omwe atsala nawo.
Masapula amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Balaka ndipo wauza Sports Torch kuti timuyi ikungofunikira zipambano zingapo kuti ichoke kumunsi komwe iwo ali.
"Tikamasewera masewero timakhala ndi cholinga chimodzi, kuti tipambane masewerowa koma apa zikuvuta tagonja, tiyesetsa mmasewero atsalawa ndi ochepa koma titapambanako 4 kapena 5 mwina titha kuchoka kumunsi, sitingapeze osewera ena kuti asewere panopa, ndi omwewa nde tingowalimbikitsa kuti aike mtima." Anatero Masapula.
Red Lions yatsala ndi masewero okwana asanu ndi atatu (8) ndipo yatsakamirabe pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe yatolera mapointsi 18.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores