KADENGE AKALOWA MMALO MWA DE JONGH
Mphunzitsi wakale watimu ya Ekwendeni Hammers, Edson Kadenge Mwafulirwa, waitanidwanso kutimu ya Silver Strikers patapita miyezi iwiri chimuimitsireni kuti akalowe mmalo mwa mphunzitsi watimuyi, Peter De Jongh, yemwe walowera mdziko la Kenya
Mmodzi mwa akuluakulu a komiti yaikulu ya timuyi, Willard Chakanika, watsimikiza za kuchoka kwa De Jong kamba koti chitupa chake chogwirira ntchito mdziko la Malawi Chatha mphamvu. Iye wati kusowa kwa ndalama yakunja kwachititsa kuti Silver ichedwe kupangitsanso chitupachi pomwe amafuna ndalama zokwana $2,000 yomwe ikukwana K2.5 million.
Kadenge, yemwe anaimitsidwa ndi timuyi kamba ka nkhani yomwe De Jongh ankati analedzera tsiku la masewero, atsogolera Mabanka mmasewero omwe akumane ndi Mighty Mukuru Wanderers mu chikho cha Airtel Top 8.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores