"MU MASEWERO A CIVO ANAWABERA, TENGANI CHITSANZO CHINA" - KAYIRA
Katswiri wakale wa timu ya Flames, Peterkins Kayira, wati chitsanzo choti timu ya FCB Nyasa Big Bullets imatha kuchokera kumbuyo ndi kupambana chisakhale ndi masewero omwe anapambana 3-2 ndi Civo kamba koti zigoli ziwiri za Bullets zinali zabodza.
Kayira amayankhula izi pa Times 360 ndipo wati zigoli za Bullets ziwiri za mmasewero awo ndi Civo zinali zabodza. Iye wati masewero omwe Bullets yagonja 1-0 ndi TP Mazembe inachita kufuna yekha.
"Kugonja kwa Bullets kunali kofuna chifukwa zolakwika zimene amapanga zinali zotheka osazipanga. Bullets inachulutsa ulemu kwambiri kuchokera pachiyambi ndipo Mazembe itapeza chigoli imatha kusewera bwino kuusintha mpira ndipo goloboyi si nthawi yogoletsetsa chigoli." Anatero Kayira.
Komabe iye wati mmene inasewera Bullets palibe timu ya mdziko muno ikanalimba ndipo ngati angakonze mavuto awo, ikhonza kukawina. Bullets ikumana ndi TP Mazembe mu masewero achiwiri pa 30 September ku DR
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores