PAJA WAMKULU AKAVUTIKA AMAMUTHANDIZIRA"" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets yachita kuthandizidwa ndi oyimbira kuti apambane mmasewero omwe matimuwa anakumana pomwe wati penate yomwe Bullets inapeza ndi yopatsidwa.
Nyambose amayankhula izi atatha masewerowa pa bwalo la Kamuzu pomwe Bullets yapambana ndi chigoli cha pa mphindi 88 za masewerowa kudzera pa penate. Iye wati timu yake yaphonya kwambiri komabe oyimbira wayithandiza Bullets.
"Ndi Zoona mchigawo choyamba tinasewera bwino kwambiri ndipo timapanga chilichonse koma mipata yathu sitinaigwiritse ntchito zomwe zinawathandiza anzathuwa kuti abweremo ndipo chigawo chachiwiri anali bwino komabe paja wamkulu ndi wamkulu akavutika amathandizidwa nde amuthandizadi." Anatero Nyambose.
Timu ya Tigers tsopano ikadali pa nambala 11 mu ligi pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores