"TINACHITAYA MU CHIGAWO CHACHIWIRI" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati kugonja kwa timu yake ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu ligi ya TNM ndi chifukwa choti mu chigawo chachiwiri sanasewere bwino.
Kajawa amayankhula izi atatha masewerowa omwe agonja 2-1 ndipo timuyi imatsogola mchigawo choyamba koma Christopher Kumwembe anamwetsa zigoli ziwiri mu chigawo chachiwiri kuti Manoma apambane. Iye wati mchigawo chachiwiri sanasewere bwino.
"Tagonja inde komabe anyamata asewera bwino, anayesetsa komabe mchigawo chachiwiri zinativuta pomwe mwina amakhutira kuti akutsogola pomwe anakhazikika kumbuyo ngakhale kuti sitinawauze zimenezo. Tivomereze kuti zativuta ndithu." Anatero Kajawa.
Kugonja kumeneko ndi koyamba kwa mphunzitsiyu kutimuyi yomwe ikadali pa nambala yachisanu ndi mapointsi 31 pa masewero 22 mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores