SALIMA SAPITA NAWO KU SAUDI ARABIA
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets yemwe ali pangongole ku Bangwe All Stars, Chikumbutso Salima, sapita nawo mdziko la Saudi Arabia kuti akayese mwayi ku timu ya Al-Faisaly pomwe Bullets yakaniza osewerayu.
Izi zadziwika ndi mkulu watimuyi, Mphatso Jika, yemwe wati Salima anaikidwa pa ndandanda wa osewera atatu omwe iwo anapemphedwa kuti apereke ndi kuti akayese mwayi koma Bullets yakaniza kamba koagwirizana ndi ndondomeko zina za ulendowu.
Osewera atatu tsopano, Robert Saizi, Emmanuel Lino komanso mtsogoleri watimuyi, Fanizo Mwansambo ndi omwe akupita pa ulendowu womwe anyamuke lolemba likudzali.
Timu ya Bangwe ikumana ndi timu ya Bullets lachitatu sabata ya mawa ndipo osewera onse omwe anachoka ku Bullets kuphatikiza Salima sadzasewera masewerowa.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores