"AWA AKHALA MAYESERO KUTI TIDZIWE POMWE TITHERE" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati masewero atimuyi pakati pa Red Lions lero komanso ndi Mighty Mukuru Wanderers lachitatu likudzali ali ngati mayesero kwa iwo kuti awaone mbali imene athere mu ligi ya chaka chino.
Kananji amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Red Lions pa bwalo la Balaka ndipo wati akuyembekeza kuti masewero awo akhala ovuta kwambiri. Iye wati akapambana masewero awo awiriwa atsimikizadi kuti satuluka mu ligi.
"Akhala masewero ovuta kamba koti tonse tikuvutika komanso titakumana pa Nankhaka tinalepherana 1-1 komabe anyamata tawauza kufunikira kopeza chipambano mmasewero awa ndi a Wanderers chifukwa ali ngati mayesero kuti tione mbali yomwe tithere. Tikapambana onse, zotuluka mu ligi sizitikhudza nawo." Kananji anafotokoza.
Timu ya Blue Eagles ili pa nambala 10 mu ligi ya chaka chino pomwe yatolera mapointsi 27 pa masewero 22 ndipo ngati ipambane lero, ifika pa nambala 10.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores