Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
OYIMBIRA NDI A BEACH SOCCER APEREKEZA HAIYA
Mabungwe awiri omwe amakhudzidwa nawo pa zisankho za bungwe la Football Association of Malawi a Oyimbira komanso a beach Soccer asankha dzina la mtsogoleri wa Super league of Malawi, Fleetwood Haiya, kuti akaime nawo ngati mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi.
Zadziwika ndi Zodiak kuti mabungwe awiriwa akufunitsitsa kuti a Haiya omwe angolowa pa mpando wa ku SULOM chaka chathachi akapikisane nawo pa mpandowu pa chisankho cha pa 16 December chaka chino.
Haiya atafunsidwa ngati ayime pa chisankhochi, sanakane kapena kuvomera koma anati ayankhapo ndipo ndi kusankhidwaku, iye akuyenera kuyimira.
Ngati iye apange chiganizo choti ayimire, mpando wake waku SULOM ndekuti awusiya ndipo utsogoleredwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr (Source: Zodiak)
MPHASI IS A FANS FAVOURITE IN ZAMBIA
Flames forward, Chifundo Mphasi, received ZK2,000 after being named as the Supporters player of the match on Saturday.
His side, Kabwe Warriors beat Green Buffaloes Football Club 3-0 to move up to the top of the table and assisted the third goal on 79th minute.
He moved to Warriors at the start of the season on loan from Shamuel Academy.
BABATUNDE SCORES HIS FIRST GOAL OF THE SEASON
Former FCB Nyasa Big Bullets forward, Babatunde Adepoju, scored his first goal of the season as Venda Football Club beat Magesi FC 2-0 in the Motsepe Foundation Championship in South Africa.
Reacting to the goal after the game, the Nigerian forward said he was happy to open his account in the new season and hopes for more goals.
"Sweet victory I'm happy to score my first goal of the season hopefully first of many to come, let the counting begin..... God over everything." Wrote Babatunde on his Facebook account.
The towering striker moved from Bullets to Venda after winning the golden boot award in the TNM Super league and Airtel Top 8.
He is married to a Malawian lady whom she has a baby for him and calls Malawi his home hence we follow him.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
SΓ³ nito eu vivo Γ©m maputu sΓ³ mecanhelano provinca do niassa
Eu vivo Γ© maputu sΓ³ mecanhelano niassa provinsi
KONDOWE MISSES BLANTYRE DERBY PARTY
FCB Nyasa Big Bullets in-form striker, Ephraim Kondowe, will not face his former club, Mighty Mukuru Wanderers, for the first time since being released by the Lali Lubani side due to suspension.
The former Wanderers Reserve captain has been the main man at the team as a substitute and now a starter but the Super League of Malawi has indicated that he has three yellow cards.
This could be Kondowe's first game in the Blantyre Derby in Bullets colours but had a taste in the big fixture after playing 5 minutes for the Nomads last year where they lost 1-2 at the Kamuzu Stadium.
He has scored 6 goals for the People's team in the TNM Super league and has been a starter in the league for the past four games.
By Hastings Wadza Kasonga Jr
Asernal
malawi
ZA KHUDA AKUTI:
Katswiriyu wathetseredwa mgwirizano kamba koti si womwetsa zigoli yemwe amamufuna pomwe akuti akutsalira kwambiri pa wosewera yemwe amamufuna.
Timu ya Tishreen SC ikufuna kuteteza chikho chimene inatenga chaka Chatha ndipo pano ali pa nambala yachisanu mu ligi ya chaka chino.
Khuda wasewera masewero anayi ndipo sanagoletse chigoli chilichonse ndipo dzulo atangosewera masewero omwe anagonja 2-0 pa kwawo, ochemerera anaonetsa kusakhutira ndi ntchito zake ndipotu patangodzutsa maola awiri, iyetu amuthetsera mgwirizano.
Akuti kusachita bwino kwa timuyi ndi Khuda komanso ndi wolemedwa kwambiri ndipo samadziwa poti azipezeka monga iye womwetsa zigoli.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"UKAMAIMBIRA BWINO OYIMBIRA ANZAKO AMADANA NAWE" - CHIZINGA
Mmodzi mwa oyimbira omwe agwira ntchito mu zaka zapitazi, Alfred Chizinga, wayankhulapo pa nkhani yomwe Oyimbira ena aku Blantyre amadandaula kuti Mwayi Msungama akukonderedwa pomwe wati ukamaimbira bwino amadana nawe.
Iye walemba izi pa tsamba lake la Facebook ndipo wati iyenso kwakumanapo nazo zoterezi komabe anakwanitsa kupita patsogolo mpaka kuimbira Blantyre derby ka 19 opanda zosokoneza.
"U Ref wa ku Malawi, ukakhala kuti ukuyimbira bwino, ndipamene ma refs anzako amayamba kudana nawe amvekere amamukondera, amapereka ndalama kwa mabwana nanga ref ndiyekhayuπ"
"I had similar situation when I was active, ndipo nditalowa pa FIFA nawo a CAF anagundika kundipansa ma games pafupipafupi ndipo ndinawanfunsa ma Dolo komanso ma ladies omwe amalumbwalumbwawo, Kodi a CAF wa akundikondelanso?? Onse adangoyakha kuti inuyo mumatha manπ." Iye analemba chonchi.
Iye wati Msungama akuyeneradi kuimbira masewero pakati pa FCB Nyasa B
HAIYA PREACHES A VIOLENCE FREE DERBY
The Super League of Malawi President, Fleetwood Haiya, has said he is expecting spectators in the much anticipated Blantyre Derby match involving FCB Nyasa Big Bullets and Mighty Mukuru Wanderers not to display violent acts in the match.
Haiya wrote this on his Facebook page on Friday ahead of the country's biggest fixture and said Violence has no part in the beautiful game of football.
"Let me appeal to all supporters of both teams to peacefully support their teams. Violence and hooliganism of any kind, has no place in our game. Together we stand for a violence free derby. Let football be the ultimate winner, as we Revive, Reform and Rebrand our elite league." Wrote Haiya.
The two sides settled for a draw in their last meeting in the first round and in their previous five meetings in the league, both sides have a win and three draws.
BULLETS RESERVE YATULUKA MUMPIKISANO WA NYASA CAPITAL FINANCE CUP
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve yatuluka mumpikisano wam'chigawo chakum'mwera wa Nyasa Capital Finance Cup, pamene yagonja masana a lero ndi timu ya Zingwangwa United ndichigoli chimodzi kwa duu mumasewero andime yachipulura yampikisanowu pabwalo la Chiwembe munzinda wa Blantryre.
Chigoli Cha Joseph Mkhuku chobwera m'chigawo chachiwiri mumphindi 76 kutsatira kulephera kuyakhulana kwa otseka kumbuyo a Bullets Reserve ndichomwe chatengera timu ya Zingwangwa United mundime yamatimu 16 mumpikisanowu.
Zateremu timu ya Zingwangwa United ikumane ndi timu ya FOMO FC mundime yamatimu 16 ampikisanowu.
Timu ya Bullets Reserve ndiyomwe yakhala ikusunga chikhochi kwadzaka dziwiiri motsogozana.
Wolemba; Frank Mojah Dzuwa
DE JONGH STILL HOPES TO WIN THE LEAGUE
Silver Strikers head coach, Pieter De Jongh, has said that his team still has hopes of winning the 2023 TNM Super League and that they will fight till the end.
The Dutch said this on Friday ahead of the team's match with Ekwendeni Hammers on Saturday which he says it will be tough but a win is a must for the Area 47 side.
"We play on Saturday at home against Ekwendeni Hammers and this is not just an ordinary game for us as we aim for a win. As usual we respect our opponents, they will come for a win as well as they want to fight relegation. So currently we haven't given up on our hope for winning the title. With the remaining games we hope to finish at 59 points," he said.
He further said he would love to play the match on Sunday to give a rest to the players but nothing can happen and they will play Hammers. After dating Ekwendeni, the Bankers will have to play Kamuzu Barracks and FCB Nyasa Big Bullets to wind up the league.
Reported by Has
"OSEWERA ATOPA KOMA SITINGACHITIRE MWINA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yawonso ikhonza kukhala ndi madando oti osewera atopa koma poti palibe chomwe chingasinthe iwo amalizitsabe kusewera.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Ekwendeni Hammers pa bwalo la Bingu loweruka ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri.
Iye wati osewera onse apezeka pomwe omwe anali ovulala achira ndipo pa nkhani ya kutopa, iye wati adziwa mongowagwiritsa ntchito mwake.
"Ndi nkhani yoti atopadi koma poti kuno ndi ku Malawi, kudandaula palibe chomwe chingasinthe nde nkhani ndi kungodziwa kuwagwiritsa osewerawa kuti onse asamatope." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver inapambana 3-1 mu chigawo choyamba pa bwalo la Mzuzu ndipo ikupita mmasewerowa ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi 50 pamasewero 27 omwe yasewera.
"KUPHA BULLETS KULIBE TANTHAUZO LILILONSE MU TNM" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati timu yake ikuyenera kuchilimika kuti ipeze chipambano pamwamba pa timu ya Dedza Dynamos pomwe wati iwo sali pabwino.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero a matimu awiriwa pa bwalo la Civo ndipo iye wati kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu Airtel Top 8 kulibe phindu poti ndi zosiyana ndi ligi ya TNM komwe kuli moyo wawo.
"Zokonzekera zikuyenda bwino ndipo tikuyembekezera masewero ovuta kwambiri poti ife sitili pabwino pomwe Dedza ikufuna kuthera mu Top 8 nde anyamata tawauza kufunikira kopambana. Za Airtel sizikugwirizana ndi za TNM nde tikuyenera kupanga za masewerowa." Anatero Makawa.
Timu ya Civo ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe ili ndi mapointsi okwana 30 ndipo ikusiyana mapointsi awiri ndi Moyale Barracks komanso Red Lions omwe ali ku chigwa cha matimu otuluka.
"NDIKUYANKHANI SABATA YA MAWA" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi, Fleetwood Haiya, wati padakali pano alibe yankho lomwe angapereke ngati ayime nawo pa chisankho cha bungwe la Football Association of Malawi ngati mtsogoleri ndipo ayankha sabata ya mawa.
Izi zadza pomwe pamveka mphekesera zoti iye apikisana nawo pa mpandowu mwezi wa mawa pomwe akulingalira zogwetsa Walter Nyamilandu Manda yemwe yakhalapo kwa zaka 19. Haiya sanakane kapena kuvomera.
"Padakali panopa ndilibe chomwe ndingakuuzeni mwina tidikire kaye sabata ya mawa ndi pomwe ndidzayankhulepo." Anatero Haiya.
Naye mtsogoleri wa FAM, Nyamilandu wati adzayankhula ngati ayimenso ikatha sabata yopereka mayina oti ayime. Haiya walowa ku SULOM mu December chaka Chatha ndipo kubwera kwake kwasintha zinthu zambiri mu ligi ya Supa ligi.
SENAJI, MWAUNGULU NDI BILIATI APEZEKA NDI WANDERERS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake ikhala ndi osewera ake, Clyde Senaji, Patrick Mwaungulu komanso Stanley Biliati mmasewero omwe akumane ndi Mighty Mukuru Wanderers lamulungu pomwe achira.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa lachisanu pomwe amapanga zokonzekera ndipo wati anyamata ake onse ali okonzeka kugwira ntchito lamulungu pa bwalo la Kamuzu.
"Tikadakonzekerabe potengera kuti tinali ndi masewero mkati mwa sabatayi ndi Lipulumundu ndipo tinapambana, dzulo tinapuma pomwe anyamata tikufuna azikhala ndi mphamvu nde lero tabwerera pa bwalo kukonza zomwe zinalakwika lachitatu. Akhala masewero ovuta poti timavutitsana nawo koma anyamata akonzeka." Watero Munthali.
Iye watsimikizanso kuti wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa, yemwe anavulala pa mphindi za masewero awo ndi Civo United mu Airtel Top 8 sapezeka kamba kovulala.
Mu chigawo choyamba matimuwa analepherana 0-0.
"MZUZU IKUFUNIKIRA BWALO NGATI LA BINGU" - NYAMILANDU
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda wauza akuluakulu a komiti yoyang'ana za Club Licensing kuti apange chiganizo pa zakutsegulidwa za bwalo la Mzuzu pasanathe masiku awiri kuyambira lero.
Nyamilandu wayankhula izi atatha kuyendera bwaloli lachinayi ndipo waonetsa kukhutira ndi ntchito yomwe khonsolo ya Mzuzu yagwira pokonza bwaloli.
"Ndilibetu vuto ndi bwaloli ndipo apa pakhonza kuseweredwa komanso akwanilitsa zonse zomwe anapemphedwa kuti achite. Padakali pano likhonza kuyamba kuchititsa masewero komabe Mzuzu likufunikira bwalo la pamwamba." Anatero Nyamilandu.
Iye wati oyendera bwaloli kuti apereke chiganizo pa bwaloli pasanathe masiku awiri. Akuluakulu a komiti ya Club Licensing anayendera bwaloli lachiwiri lathali.
Source: Times
"TASEWERA BWINO KWAMBIRI NDI BULLETS" - NKHOMA
Mphunzitsi watimu ya Lipulumundu FC, Limbani Nkhoma, wati samayembekezera kuti timu yake isewera mwapamwamba ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati ndi wokhutira ndi anyamata ake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati anyamata ake anachilimikira poyimitsa Bullets mchigawo chonse choyamba.
"Anyamata asewera bwino kwambiri ndipo sindimayembekezera kuti angachite chonchi, kungogonja 2-0 yokha basi komanso zigoli za chigawo chachiwiri ndekuti anyamata anagwira ntchito nde ineyo ndine wokondwa ndi mmene asewerera." anatero Nkhoma.
Timu ya Bullets inapeza zigoli kudzera mwa Thomson Magombo komanso Chawanangwa Gumbo kuti ifike mu ndime ya matimu 32 a chikho cha Castel Challenge Cup. Lipulumundu imasewera mu Division One ya ku mmwera ndipo kwawo ndi ku Mangochi.
"TILIMBIKIRA MASEWERO OMWE ATSALAWA" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu yake ilimbikira masewero awo omwe atsala nawo kuti mwina angathe kutsala mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Ekwendeni Hammers 1-0 ndi chigoli cha Humphreys Minandi ndipo wati ananena kale kuti ligi siyinathe.
"Tithokoze osewera athu kamba kosewera mwapamwamba, tithokozenso Mulungu kamba ka chipambanochi, ndinkanena kuti ligi siyinathe nde apapa tangotsala ndi masewero awiri nde tiwakonzekere bwino kuti tichite bwino." Anatero Masapula.
Patsogolo pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets, iye wati awakonzekera masewerowa poti kutola mapointsi mmasewerowa kudzawachitira ubwino waukulu. Iwo adakali pa nambala 15 ndi mapointsi 28 pamasewero 28 amu ligiyi.
"TIZIBWANA PANG'ONO TATIPWETEKETSA" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati timu yake inangochita zibwana pang'ono zomwe zachititsa kuti agonje pomwe amasewera ndi Red Lions.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Balaka ndipo wati timu yake inali bwino mchigawo choyamba koma Lions inasintha zinthu mu chigawo chachiwiri.
"Anali masewero a zigawo ziwiri, mu chigawo choyamba tinasewera bwino moti tinapeza mipata yochuluka yoti tikanatha kugoletsa koma chigawo chachiwiri Red Lions inabwera, analowetsa winawake kumbaliku yemwe anasinthadi zinthu, ndi tizibwana tinachinyitsa." Anatero Mauluka.
Timu ya Ekwendeni Hammers tsopano ili nawo pa ngozi yoti itha kutuluka mu ligi ya TNM pomwe ili ndi mapointsi 30 pa masewero 27 ndipo ali pa nambala 13 mu ligiyi.
"IKANAKHALA LIGI YATHA SIBWENZI TIKUMENYA MASEWERO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake ikuyang'anabe mwachidwi masewero awo omwe akusewera ndipo wati ligi siyinathe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa timu ya Chitipa United 1-0 pa bwalo la Karonga ndipo wati ndi okondwa kamba koti akhala timu yoyamba kugonjetsa Chitipa pa kwawo.
"Ndife okondwa kamba koti tapambana, awa ndi masewero oyamba kugonja panopa koma tasewera bwino, tinapeza mipata yochuluka komabe tapeza chigoli cha changu. Chilichonse chikhonza kuchitika, ikanakhala kuti ligi yatha sibwenzi tikusewerabe masewero." M'gangira anafotokoza.
Timu ya Silver Strikers tsopano ili ndi mapointsi okwana 50 pa masewero 27 omwe yasewera ndipo ili pa nambala yachitatu mu ligiyi.
"AKUYENDETSA MPIRAWA ANGONENA CHOMWE AKUFUNA" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati ndi wokhumudwa kamba ka omwe amapanga masewero akuchitira pomwe ayipanikiza timuyi ndi masewero ambiri ngakhale kuti kutsogoloku kuli mpata wambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya Silver Strikers pakwawo ndipo wati omwe amapanga masewerowa angonena chimene akufuna.
"Anyamata anga asewera bwino koma zomwe tikunena kuti mtima ukufuna koma mtima ukukana, tinapita ku Blantyre anati tipite ku Lilongwe kokamenya ndi Civo kenaka tikubwera kuno ati tikhote kaye ku Rumphi apa akuti tibwererenso ku Rumphi kokumana ndi Moyale, anthuwa ndi matupi amafuna kupuma." Anatero Mtetemera.
Iye wati ndi wokondwa poti khumbo lawo la chaka chino layenda ndipo ali pa nambala yachinayi ndi mapointsi 44 pa masewero 27 mu ligi.
Bullets 8_0lipumundu
Silver strikers
"MMENE ZIKUYENDERA SIZIKUNDIKONDWERETSA" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati sakukondwa ndi mmene timu yake ikupatsidwira masewero osiyanasiyana zomwe zikuchititsa kuti osewera azitopa.
Nginde amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Silver Strikers pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake sikupatsidwa ulemu popereka masewero.
"Kunena zoona masewero tikusewera pafupifupi ndipo anyamata tsopano akutopa nanga taonani chichokereni kunyumba popita ku Blantyre tinadutsa ku Rumphi mpaka pano sitinafike nde mmene zilili sizikundikondweretsa ndipo sakutipatsa ulemu ndi mmene akuchitira." Anatero Mtetemera.
Kumbali ya masewero, iye wati chilichonse chikhonza kuchitika pa bwalo la zamasewero. Chitipa United ili pa nambala yachinayi ndi mapointsi 44 pa masewero 27.
"SILVER NGATI TIMU YAIKULU IMAFUNIKIRA PA 1 KAPENA 2" M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati kupambana mmasewero awo omwe akusewera ndi timu ya Chitipa United lachitatu ku Karonga ndi kufunikira poti iwo ngati timu yaikulu amafunikira kukhala pabwino.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri.
"Takonzekera kwambiri pa masewero amenewa kutengera kuti tinataya mapointsi ndi Karonga koma osewera amadziwa kuti akamachita bwino amapeza ndalama nde kupambana ndi Chitipa kukhala kofunika kwambiri."
"Mukudziwa kuti Silver Strikers ndi timu yaikulu nde ngati timu yaikulu tikuyenera kumakhala pa nambala yoyamba kapena yachiwiri nde kupambana nkofunika." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi okwana 47 pa masewero 26 omwe yasewera.
AWIRI AMANGIDWA KAMBA KOONETSA MASEWERO MOPANDA CHILOREZO
Abambo awiri, Lapken Thole komanso Samson Chikwata, akuimbidwa mlandu ndi bungwe la Super League of Malawi kamba kojambula masewero a mpira wamiyendo a pansi mwa bungweli mopanda chilolezo.
Awiriwa apatsidwa mlandu wozizimbayitsa ngati ma membala opatsidwa mphamvu pansi pa bungwe zomwe ndi zosemphana ndi Section 101 ndi 102 ya malamulo a kufalitsa nkhani.
Iwo apatsidwa mlanduwu ndi khothi la majesitileti ku Blantyre ndipo apatsidwa belo la polisi. Iwo ankaonetsa masewero a FCB Nyasa Big Bullets komanso Kamuzu Barracks sabata yatha pa tsamba la mchezo.
Bungweli lachenjeza anthu onse kuti kuonetsa masewero aliwonse a pansi pa bungweli mopanda chilolezo chawo ndi mlandu ndipo lamulo lidzagwira ntchito pa onse opekeza.
ATATU ALIMBIRANA MPHOTO YA KU BULLETS
Osewera atatu, Ephraim Kondowe, Precious Phiri komanso Rabson Chiyenda, asankhidwa kuti apikisane pa mphoto ya wosewera wapamwamba kuposa onse mu mwezi wa October kutimuyi.
Timuyi yatulutsa mayinawa lachiwiri kudzera pa tsamba lawo la mchezo ndipo Kondowe akhonza kupambana mphotoyi kachiwiri atapambana ya mwezi wa September.
Naye Phiri komanso Chiyenda apezekapo koyamba kenikeni pomwe Phiriyu anakhala ofunikira kwambiri polowa mmalo mwa omwe anali ovulala ndipo Chiyenda waziguliranso malo a pagolo atasowa kwa nthawi yoyamba.
Mu mweziwu, Bullets yapambana chikho cha FDH Bank Cup, kufika ndime Ina ya chikho cha Airtel Top 8 komanso kufika pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM.
LIONEL MESSI WINS RECORD-EXTENDING EIGHTH BALLON DβOR AWARD
The winner of the 2023 Ballon dβOr has been announced and Lionel Messi has won a record-extending eighth award. The Inter Miami and Argentina striker, who played for Paris Saint-Germain last season, captained Argentina to the World Cup in Qatar last December, ending a 36-year wait for the South American country. Messi, 36, has won the award three times more than anyone else.
Ballon dβOr top three ranking: 1οΈβ£ Lionel Messi 2οΈβ£ Erling Haaland 3οΈβ£ Kylian MbappΓ©.
Players
Manoma atsala ndi magemu angati
"TINALI NDI MIPATA YAMBIRI YOTI TIKANATHA KUPAMBANA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yapeza point imodzi pamwamba pa timu ya Silver Strikers ndipo wati ziwathandiza mmasomphenya awo omaliza pabwino.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo anati anyamata ake anasewera bwino kuposa Silver Strikers.
"Anali masewero abwino kwambiri, kuimitsa timu ngati Silver Strikers ndekuti anyamata achita bwino kwambiri. Tinali ndi mipata yambiri yoti tikanatha kupeza zigoli, Silver inangopeza mpata umodzi mchigawo chachiwiri komabe point imodzi ndi yabwino." Anatero Kajawa.
Iye anati pa masewero atatu omwe atsala nawo ndi FCB Nyasa Big Bullets, Bangwe All Stars komanso Mighty Wakawaka Tigers, ayesetsa kuti achite bwino. Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi 37 pa masewero 27.
"BWALO SILABWINO SITIKANAMENYA MPIRA WATHU" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake inayesera kusintha kaseweredwe kamba koti bwalo la Karonga silabwino koma zinavutabe ndipo wati ndi zowawa kufanana mphamvu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi Karonga United ku Karonga ndipo anati anali masewero omwe akanatha kupambana mosavuta koma aphonya kwambiri.
"Kusintha kumene tinasintha ndi chifukwa choti bwaloli silabwino, sitikanatha kupatsirana ndi kumenya mpira wathu mpake tinalowetsa osewera ataliatali komabe taphonya kwambiri ndi zotsatira zowawa kwambiri." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi okwana 47 pamasewero 26 omwe asewera mu ligi ya TNM.
"SITINALI BWINO NDIPO WANDERERS INALI BWINO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake sinali bwino ndipo kunali kovuta kugonjetsa Wanderers poti inasewera bwino pali ponse.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo anati mmasewero omwe atsala ayesetsa kuti achite bwino kuti athere mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi.
"Masewero ativuta kwambiri sitinasewere bwino ndipo anyamata nawo sanali bwino. Wanderers imakhalitsa ndi mpira komanso mipata yomwe anayipeza agwiritsa ntchito." Anatero Mkandawire.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe yatolera mapointsi okwana 35 pa masewero 27 omwe yasewera mu ligiyi.
"WE'D HAVE WIN THE LEAGUE IF WE PLAYED LIKE THIS" - HARRISON
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, was pleased with how his team played when they beat Bangwe All Stars 3-0 at the Kamuzu Stadium and said they could have won the league very easy.
Harrison said this after the match that the win automatically puts them on a safe position in a title race and it was a bright performance ahead of the much anticipated Blantyre Derby with FCB Nyasa Big Bullets.
"We dominated the game from the first whistle to the last, that performance we've been looking for for a long time and I know that the players could do and we have to bring that performance from game to game. If we had done that the whole season, we could have win the league." Said Harrison.
The win has put the Nomads on level with FCB Nyasa Big Bullets on second in the table with 53 points from 27 games and the people's team have three games in hand.
MPINGANJIRA WADYETSA BWINO OSEWERA A NOMA
President wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, apereka ndalama zokwana K200,000 kwa osewera asanu ndi mmodzi kwa aliyense kamba kochita bwino mmasewero omwe anasewera sabata yangothayi.
Iye wapereka ndalamazi kwa magoloboyi awiri, William Thole komanso Dalitso Khungwa, kamba kosagoletsetsa zigoli mmasewero awo ndi Bangwe All Stars komanso FOMO.
Osewera monga Christopher Kumwembe, Wisdom Mpinganjira, Peter Cholopi komanso Chiukepo Msowoya apatsidwa K200,000 kamba komwetsa zigoli mmasewero awiriwa.
Wanderers inagonjetsa FOMO 1-0 mu Castel Challenge Cup lachinayi isanagonjetse Bangwe All Stars 3-0 mu ligi ya TNM.