"SITINALI BWINO NDIPO WANDERERS INALI BWINO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati timu yake sinali bwino ndipo kunali kovuta kugonjetsa Wanderers poti inasewera bwino pali ponse.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo anati mmasewero omwe atsala ayesetsa kuti achite bwino kuti athere mu matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi.
"Masewero ativuta kwambiri sitinasewere bwino ndipo anyamata nawo sanali bwino. Wanderers imakhalitsa ndi mpira komanso mipata yomwe anayipeza agwiritsa ntchito." Anatero Mkandawire.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe yatolera mapointsi okwana 35 pa masewero 27 omwe yasewera mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores