"NDIKUYANKHANI SABATA YA MAWA" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi, Fleetwood Haiya, wati padakali pano alibe yankho lomwe angapereke ngati ayime nawo pa chisankho cha bungwe la Football Association of Malawi ngati mtsogoleri ndipo ayankha sabata ya mawa.
Izi zadza pomwe pamveka mphekesera zoti iye apikisana nawo pa mpandowu mwezi wa mawa pomwe akulingalira zogwetsa Walter Nyamilandu Manda yemwe yakhalapo kwa zaka 19. Haiya sanakane kapena kuvomera.
"Padakali panopa ndilibe chomwe ndingakuuzeni mwina tidikire kaye sabata ya mawa ndi pomwe ndidzayankhulepo." Anatero Haiya.
Naye mtsogoleri wa FAM, Nyamilandu wati adzayankhula ngati ayimenso ikatha sabata yopereka mayina oti ayime. Haiya walowa ku SULOM mu December chaka Chatha ndipo kubwera kwake kwasintha zinthu zambiri mu ligi ya Supa ligi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores