ATATU ALIMBIRANA MPHOTO YA KU BULLETS
Osewera atatu, Ephraim Kondowe, Precious Phiri komanso Rabson Chiyenda, asankhidwa kuti apikisane pa mphoto ya wosewera wapamwamba kuposa onse mu mwezi wa October kutimuyi.
Timuyi yatulutsa mayinawa lachiwiri kudzera pa tsamba lawo la mchezo ndipo Kondowe akhonza kupambana mphotoyi kachiwiri atapambana ya mwezi wa September.
Naye Phiri komanso Chiyenda apezekapo koyamba kenikeni pomwe Phiriyu anakhala ofunikira kwambiri polowa mmalo mwa omwe anali ovulala ndipo Chiyenda waziguliranso malo a pagolo atasowa kwa nthawi yoyamba.
Mu mweziwu, Bullets yapambana chikho cha FDH Bank Cup, kufika ndime Ina ya chikho cha Airtel Top 8 komanso kufika pa nambala yoyamba mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores