SENAJI, MWAUNGULU NDI BILIATI APEZEKA NDI WANDERERS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake ikhala ndi osewera ake, Clyde Senaji, Patrick Mwaungulu komanso Stanley Biliati mmasewero omwe akumane ndi Mighty Mukuru Wanderers lamulungu pomwe achira.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa lachisanu pomwe amapanga zokonzekera ndipo wati anyamata ake onse ali okonzeka kugwira ntchito lamulungu pa bwalo la Kamuzu.
"Tikadakonzekerabe potengera kuti tinali ndi masewero mkati mwa sabatayi ndi Lipulumundu ndipo tinapambana, dzulo tinapuma pomwe anyamata tikufuna azikhala ndi mphamvu nde lero tabwerera pa bwalo kukonza zomwe zinalakwika lachitatu. Akhala masewero ovuta poti timavutitsana nawo koma anyamata akonzeka." Watero Munthali.
Iye watsimikizanso kuti wotseka kumbuyo, Gomegzani Chirwa, yemwe anavulala pa mphindi za masewero awo ndi Civo United mu Airtel Top 8 sapezeka kamba kovulala.
Mu chigawo choyamba matimuwa analepherana 0-0.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores