MPINGANJIRA WADYETSA BWINO OSEWERA A NOMA
President wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, apereka ndalama zokwana K200,000 kwa osewera asanu ndi mmodzi kwa aliyense kamba kochita bwino mmasewero omwe anasewera sabata yangothayi.
Iye wapereka ndalamazi kwa magoloboyi awiri, William Thole komanso Dalitso Khungwa, kamba kosagoletsetsa zigoli mmasewero awo ndi Bangwe All Stars komanso FOMO.
Osewera monga Christopher Kumwembe, Wisdom Mpinganjira, Peter Cholopi komanso Chiukepo Msowoya apatsidwa K200,000 kamba komwetsa zigoli mmasewero awiriwa.
Wanderers inagonjetsa FOMO 1-0 mu Castel Challenge Cup lachinayi isanagonjetse Bangwe All Stars 3-0 mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores